0,"Tiyi ndi imodzi mwa mbewu zothandiza ku mwera ndi kum'mawa kwa Afilika, ndipo imathandiza alimi ambiri kupeza ndalama"
1," Koma ngati alimi satsatira ndondomeko yoyenerera pa ulimi wa mbewuyi, chilengedwe, madzi ndi nthaka zimawonongeka, komanso ogwira ntchito pa mundapo amavutika"
2, Choncho ulimi wa tiyi umenewo si umapitiliranso
3,Kugwiritsa ntchito mankhwala si njira yokhayo yotetezela mbewu ku tizilombo ndi matenda
4," Ngati tiyi akusamalidwa bwino mu Afilika, atha kupilira ku tizilombo popanda kuthira mankhwala"
5, Kupopera mankhwala kukhoza kuwononga chitetezo cha mbewu ndikupangitsa kuti matenda ayambe
6," Mu gawo limeneli, tiphunziramo za m'mene tingapewere matenda ndi tizilombo"
7,"Ngati mwabzala phata latsopano la tiyi, musankhe mbewu za tiyi zomwe zimapilira ku matenda ndi tizilombo tomwe timaononga tiyi"
8, Ndibwino kubzala mbewu zambiri za tiyi osakhala imodzi yokha
9," Ngati mwabzala mbewu za tiyi zosiyana, muzibzale mtundu uliwonse padera kuti musavutike pozisamalira"
10,"Ngati mundawo unagwidapo ndi matenda owononga mizu, matendawa atha kukhala kuti atsalira mu mitengo imene idakali m'mundamo"
11," Choncho, ndikoyenera kuti matendawa athetsedwe pogwiritsa ntchito njira yosadzula mitengo"
12, Iyi ndi njira imene mumasadzula makungwa a mtengo
13,Kuphimba tiyi komanso kuonetsetsa kuti phata la tiyi liri pa mlingo wabwino zimathandizila kuti dzuwa lisaombe pa nthaka
14, Izi zimathandizira kuti zomera zosafunikira zisamele
15, Ndibwino kupalira ndi manja chifukwa kupalira ndi khasu kumathanso kuwononga mizu ya tiyi
16,Mbewa zomwe zimaononga mitsitsi ya tiyi
17, Mbewa zikhoza kupewedwa pokumba Mayenje komanso pobzala mbewu zina zimene zimathamangitsa tizilombo
18," Mbewu zimenezi ndi monga Mthuthu (Tephrosia vogelli- mtundu wa chomera umene umagwiritsidwa ntchito yopangila mankhwala a m'munda), Tagetes minuta (mtundu wa chomera umene uli mgulu la mpendadzuwa), anyezi ndi adyo"
19,"Ngati mukuwona kuti mitengo ili ndi ti zilonda pa tsinde ndi nthambi, dziwani kuti izi ndi zizindikiro za matenda owoletsa mitengo"
20, Awa ndi matenda amene amagwira mtengo kudzela mu tizilonda timene timadza chifukwa chakuti mtengo wakhapidwa
21, Mtengo utha kukhapidwa pamene mukupalira ndi khasu komanso tizilombo ndi makoswe zitha kubowola mtengo
22,"Kuti muthane ndi udzudzu wa tiyi, mukuyenera kutchola masamba anthete a tiyi ndikusiya masamba okhwima"
23," Potchola masamba onse anthete amene amadyedwa ndi udzudzu wa tiyi, zimathandiza kuti udzudzuwu usapitilire"
24," Kuti mupewe matenda a udzudzu wa tiyi, ndibwino kubzala mitundu ya mbewu ya tiyi imene imapilira ku udzudzu wa tiyi"
25,Mbalame zina zimadya tizilombo ndikuchepetsa chiwerengero chatizilomboti
26, Mukapopela mankhwala tizilombo pamodzi ndi mbalame zomwe zimafa
27," Posapopela mankhwala, mumateteza mbalamezi zimene zimathandiza pochepetsa tizilombo"
28,"Mukatha kupopera mankhwala, muyenera kutsuka zipangizo zothiririra mankhwala ndi zozitetezera"
29," Madzi otsukira amatsalira mankhwala, ndiye ngati simusamala, akhoza kuononga chilengedwe"
30,"Mukapopera mankhwala m'madimba a masamba, tsukani zida ndikuthira madzi m'dimba momwemo"
31,"Mukapopera mankhwala zifuyo, tsukani zida ndikutaya madzi mdzala/mdzenje"
32, Mdzenje muyenera kudzadza makala omwe amathandiza kuyeretsa madzi
33, Osadula mitengo yachilengedwe kuti mupange makala
34, Kumbukiraninso kuchapa zovala zozitetezera
35, Madzi ochapira atayidwe monga tafotokozera pamwambapa
36,"Ngati madzi okutha ntchito ali ochepa, akhoza kutayidwa mungalande yokumbidwa kumbuyo kwa dimba"
37, Ngalande idzalidwe ndi nthochi ndi mizu yomwe imamwa madzi ambiri
38,"Mitengo ya bulugama imapereka nkhuni, koma ikabzalidwa pamalo ponyowa, mtsinje kapena chitsime, imamwa madzi ambiri mpaka kuumitsa madzi"
39," Ngati mtsinje kapena chitsime ziuma, zingathe kukhudza miyoyo ya apabanja panu ndi anthu amudera mwanu"
40, Tikuyenera kuteteza magwero a madzi
41,"Madzi ndi moyo, choncho timafuna madzi okwanira pa miyoyo yathu"
42, Njira ina yopezera madzi yosavuta ndi kukolola madzi a mvula
43, Mungakolole madzi a mvula amene amagwa pa denga nkuwasunga mu thanki
44, Mukhoza kuwagwiritsa ntchito madzi amenewa mnyumba mwanu pokumwa koma mutawawiritsa kaye
45," Mvula ndi gwero lodalirika la madzi, choncho tidziwe mmene tingawagwiritsire ntchito madzi athuwo"
46,"Kutentha kumaononga manyowa ndi tizilombo tobwezeretsa nthaka mudothi, zomwe zimagugitsa nthaka"
47, Kutentha pokonza malo ndikoletsedwa
48,"Mukhitchini mukakhala mopanda potulukira utsi, utsi otsala muchipinda ukhoza kudzetsa mavuto azaumoyo, kuononga mapapo ndi maso a ogwira ntchito ndi mabanja awo"
49, Khitchini yapotulutsira utsi imateteza umoyo wawo ndipo imatukula miyoyo ya ogwira ntchito
